Satana Kutsutsana ndi KRISTU - Chichewa
• Pali kupambana kwakukulu polimbana ndi mizimu yoipa.
• Osapembedza Satana, wonyenga wonyengayo, kapena mizimu yoipa.
• Onse olandira "chizindikiro cha chirombo" pamphumi pao, kuti agule kapena kugulitsa, adzatayidwa kwamuyaya.
Kolembedwa ndi Watson Goodman KaulereOsagulitsa
Satana Kutsutsana ndi KRISTU
Satana yemwe m'Bukhu Lopatulika limamunena kuti
"mfumu ya dziko lapansi," ndi mdani wamkulu wa Mulungu komanso munthu
yemwe ndi wopambana pa zolengedwe zonse. Anthufe tiri pa malo ovuta kwambiri
pomwe tikumenyana ndi Satana tisankhe pakati pa Ambuye awiriwa kuti
adzatitsogolera mpaka muyaya ndi mdani KRISTU mlengiyemwe ndi Imanueli
(Mulungu nafe)kapena Satana, wolengedwayemwe ndi mfumu youkila Mulungu.
Kupyolera mu imfa ndi kuuka kwake, KRISTU anawagonjetsera onse omwe
amamukhulupilira iye.
Satana amayesa kunyenga ndi kusocheretsa anthu. Chipembedzo ndi nkhani yaikuru. KRISTU, mlengi wathu, ayenera kupembedza. Tiyenera kufanana ndi iye yemwe tipembedza. Njira ya Satana zonyengera anthu ndizo: 1) kusadalira Mulungu, 2) kumvera ziwanda, 3) kupembedza "munthu wochimwa", 4) kupembedza "chifanizo chake", ndipo 5) chizindiro cha pathupi choyenereza kuti munthu agule ndi kugulitsa. Chenjerani ndi zimenezi! Watson Goodman
MULUNGU SANALENGA MUNTHU WOTSUTSANA NAYE 1
Mulungu Analenga Lusifara kuti
Akhale"...Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi cizindikilo, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro. Unali m'Edene, munda wa Mulungu, mwala uli wonse wa mtengo wace unali copfunda cako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golidi; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu."
Anali pafupi ndi mpando
wachifumu wa Mulungu"Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto."
Analengedwa Wangwiro
"Unali wangwiro m'njira zako cilengedwere iwe, mpaka cinapezeka mwa iwe cosalungama."
Mulungu Amatulutsa Tchimo
"Mwa...malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto." —Ezekieli 28:12-16
CHINAYAMBITSA KUTI LUSIFARA ACHIMWE NDI CHIYANI? 2
Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa. —Miyambo 16:18
"Unadzikuza mtima cifukwa ca kukongola kwako, waipsa nzeru zako; cifukwa ca kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye." —Ezekieli 28:17
Tsoka La Munthu Wogalukira
"Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona. Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka coopsa, ndipo sudzakhalanso konse." Ezekieli 28:18, 19
Olengedwa Onse Amvere Namalenga
Tumikirani Yehova ndi cikondwerero: Idzani pamaso pace ndi kumyimbira mokondwera. Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ace; Ndife anthu ace ndi nkhosa za pabusa pace. —Masalmo 100:2, 3
LUSIFARA ANADZINENERA YEKHA KUTI ANALI WODZIDALIRA YEKHA 3
"Wagwadi kucokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbanda kuca! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu! Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wacifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto; ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba."
Wodzetsa Chionongeko pa
Dziko Lapansi"Koma udzatsitsidwa kunsi ku manda, ku malekezero a dzenje. ............
Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu; amene anapululutsa dziko, napasula midzi yace, amene sanamasula ndende zace, zinke kwao?"
"Mafumu onse a amitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwace. Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati cobvala ca ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira ku miyala ya dzenje...." Yesaya 14:12-19
KUSATSAMIRA PA MULUNGU NDI KOOPSYA 4
Choyamba mwa Lusifara
Yesu anaëauza kuti, "Ndinaona Satana alikugwa kuchokera Kumwamba ngati mphezi." Luka 10:18
Mwa Angelo Otsatira Satana
...Mulungu sanalekerere angelo amene anachimwa aja, koma anaëaponya m'ndende, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo. 2 Petro 2:4
Satana Amalamulira Anthu
...Poti munthu amasanduka kapolo wa chimene chamugonjetsa. 2 Petro 2:19
"Chifukwa kudzaoneka anthu onena monama kuti iwo ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena kuti ndi aneneri. Azidzachita zizindikiro zodabwitsa ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeretse ngakhale anthu amene Mulungu anaëasankha." Mateo 24:24
Kumwamba Kuyenera Kukhala
Chifuniro ChimodziMusamatsanzira makhalidwe oipa a dziko lino lapansi, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziëa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondweretsa. Aroma 12:2
ZOMUYENERA MULUNGU PA CHIPEMBEDZO CHONSE 5
"Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakuturutsa m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo. Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha." —Deuteronomo 5:6, 7
Mcitireni Yehova ulemerero wa dzina lace; bwerani naco copereka, ndipo fikani pamaso pace; lambirani Yehova m'ciyero cokometsetsa. 1 Mbiri 16:29
"...Pembedzani Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja, ndiponso akasupe a madzi." Chibvumbulutso 14:7
Koma Yesu anati, "Choka, Satana! Malembo akuti, `Uzipembedza Ambuye Mulungu wako, ndipo uzitumikira Iye yekha.' " Mateo 4:10
Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga. (Onani Genesis 1:27.) Masalmo 95:6
Anthu Onyengedwa
Amapembedza Woukira...Anthu onse anatsata chilombo chija alikudabwa. Anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Anapambedzanso chilombo chija. ... Chibvumbulutso 13:3, 4
MUSAPEMBEDZE OTSUTSANA NDI MULUNGU 6
Satana Ndi Mizimu Yake
Amalakalaka ChipembedzoPotsiriza Satana anatenga Yesu napita naye paphiri lalitali kwambiri. Anamuonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wawo, namuuza kuti, "Zonsezi ndidza- kupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza." Mateo 4:8, 9
Anthu ena onse otsala, amene sanaphedwe ndi miliri ija, sanalape ndi kusiya zimene anapanga ndi manja awo. Sanaleke kupembedza ziëanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda. Chibvumbulutso 9:20
Mulungu Amaononga Anthu
Opembedza Motere...Ndipo zironda zonyansa ndi zopweteka zinabuka pa anthu onse aja, amene analandira chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake....Aliyense anaweruzidwa molingana ndi ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiëiri. Chibvumbulutso 16:2; 20:13, 14
Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa. Yesaya 42:8
ANGELO A KRISTU NDI ANGELO A SATANA 7
Angelo A Mulungu Ndi
Amphamvu Koposa Angelo A SatanaLemekezani Yehova, inu angelo ace; a mphamvu zolimba, akucita mau ace, akumvera liu la mau ace. Masalmo 103:20
Ndipo kunabuka nkhondo Kumwamba. Mikaele ndi angelo ake anachita nkhondo ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chinatengana nawo, koma sichinapambane.... Chibvumbuluto 12:7, 8
Nanga angelo, si ndiwo mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha iwo amene adzalandire chipulumutso? Aheberi 1:14
Pakuti adzalamulira angelo ace za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Masalmo 91:11, 12
Angelo A Satana (Mizimu Yoipa)
Ndi Olimba MtimaMzimu Woyera alikunena momveka kuti pamasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo. Adzamvera anthu onyenga, nadzatsata ziphunzitso zochokera kuziëanda. 1 Timoteo 4:1
ANTHU KOMANSO ZINTHU ZIMENE SATANA AMADANA NAZO 8
Munthu, Wolengedwa
M'chifuniro Cha MulunguPamene mwanayo analikubwera, chiëandacho chinamgwetsa pansi ndi kumgwedeza kolimba. Koma Yesu anadzudzula chiëanda chonyansacho, ndipo atachiritsa mwanayo, anamperekanso kwa bambo wake. Luka 9:42
Kristu (Mulungu) Wokhala Ndi
ChipulumutsoPamene Herode...anakwiya kwambiri. Anatuma anthu ku Betelehemu ndi kumalo ake onse ozungulira, kuti akaphe ana amuna onse a zaka ziëiri ndi ocheperapo. Zaka zimenezi ndi monga iye anafunsitsira kwa akatswiri a nyenyezi aja. Mateo 2:16
Mau a Mulungu Satana
Amawatsutsa Mau A Mulungu..."Ea! kodi anatitu Mulungu,...?" Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, "Kufa simudzafai."Genesis 3:1, 4
Okhulupilira Obadwa Ndi Mzimu
...Mdani wanu Satana amayendayenda ngati mkango wobangula namafunafuna woti amudye. 1 Petro 5:8
SATANA, WOTSANZIRA 9
Satana Amatsanzira Zizindi-kiro Monga Mwini
Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza. Iwo adzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala lolembedwa pamphumi pawo. Chibvumbulutso 22:3, 4
(Onani kutsanzira kwa Satana, tsamba la 35.)
Aipsya Uthenga Wabwino
Ndi Kunena BodzaNdilikudabwa kuti mulikupatuka msangamsanga motere kusiya Mulungu, amene anakuitanani mwa kukoma mtima kwake, ndipo kuti mulikutsata uthenga wabwino wina. Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene alikukusokonezani, ndipo alikufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Kristu. Galatia 1:6, 7
Amatsanzira Aneneri A
MulunguAnthu otereëa sali atumwi oona, koma ndi antchito onyenga, amene amadzizimbaitsa, naoneka ngati atumwi a Kristu. Si zododometsa zimenezi ayi, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. 2 Akorinto 11:13, 14
DZIPATULENI NOKHA KU MAFANO 10
Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano. 1 Yohane 5:21
"Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo...." Eksodo 20:3-5
Milungu Yina Ndi Yonyansa
Pamaso Pa Mulungu."Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri atali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri. Dzicenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu....Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti ziri zonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazicitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao." Deuteronomo 12:2, 30, 31
...Kodi ndipereke...cipatso ca thupi langa cifukwa ca kucimwa kwa moyo wanga? Mika 6:7
Mwazi wa Yesu Kristu umachotsa machimo athu.
KUPUSA KWA KUPEMBEDZA MAFANO 11
Anasiya zoona za Mulungu natsata zabodza. Anapembedza natumikira zolengedwa, m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene tiyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen. Aroma 1:25
Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; acita ciri conse cimkonda. Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi, nchito za manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao. Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira. Masalmo 115:3-8
Kupembedza Mafano Ndiko
Kupembedza Mizimu Yoipa, Kapena Satana...Peëani kupembedza mafano. Iyayi koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa ziëanda, osati kwa Mulungu. ... 1 Akorinto 10:14, 20
Chilango Chobwera
Chifukwa Chopembedza Mafano"...Opembedza mafano,...malo awo ndi m'nyanja yamoto woyaka ndi miyala ya sulufure. Imeneyi ndiyo imfa yachiëiri." Chibvumbulutso 21:8
MULUNGU AMADANA NDI KUPEMBEDZA MAFANO 12
Mulungu Anaononga Mitundu
Cifukwa Cha Mafano"...Palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga. Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golidi ziri pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu. Musamalowa naco conyansaci m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi naco...." Deuteronomo 7:24-26
Cifukwa ninji panali A'Israyeli ambiri amene anagwidwa ndi mizimu yoipa pamene Kristu analalikira padziko lapansi? Cifukwa akholo awo anapembedza mizimu yoipa!
Ndipo anatumikira mafano ao, Amene anawakhalira msampha: Ndipo anapereka ana ao amuna ndi akazi nsembe ya kwa ziwanda, potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ace, Nanyansidwa Iye ndi colowa cace. Masalmo 106:36, 37, 40
Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine. Eksodo 20:5
UFITI ULI WONSE NDI TCHIMO 13
"Wanyanga usamlola akhale ndi moyo." Eksodo 22:18
"Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao...." Levitiko 19:31
Ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi. Mika 5:12
"Pakuti kupanduka kuli ngati coipa ca kucita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yacabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu." 1 Samueli 15:23
"Mutakalowa m'dziko limene Ye- hova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kucita monga mwa zonyansa za amitundu aja. Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wace wamwamuna kapena mwana wace wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza ali yense wakucita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo cifukwa ca zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu." Deuteronomo 18:9-12
Matsenga: Kunena za mtsogolo poombeza maula ndi kukhulupilira mizimu ya anthu akufa.
KUNENA ZA MTSOGOLO POTHANDIZIDWA NDI MIZIMU YOIPA 14
Mulungu Amaletsa Nyanga,
Kuombeza Maula ndi Kudzitema Mphini"Musamadya kanthu ndi mwazi wace; musamacita nyanga, kapena kuombeza ula. Musamadziceka matupi anu cifukwa ca akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova." Levitiko 19:26, 28
"Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu...." Yeremiya 27:9
"...Ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi acigololo, ndi olumbira monama...." Malaki 3:5
Pakuti aterafi anena zopanda pace, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto acabe, asangalatsa nazo zopanda pace; cifukwa cace ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa. Zekariya 10:2
Khulupirirani Mbusa Weniweni
[Yesu anati,] "Mtima wanu usabvutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso." Yohane 14:1
Matsenga: Kuneneratu za mtsogolo zomwe ndi zosadziwika pogwiritsa ntchito njira zonama.
Tsenga: Mizimu yoipa ichita tsenga.
MUTSUTSE NJIRA ZONSE ZOCHITIRA MAULA 15
Kucita Matsenga Ndi Mizimu
Yodziwika BwinoNdipo pamene iwo adzati kwa iwe, "Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza," kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao?... Yesaya 8:19
Kugwiritsa Ntchito Ziwalo
Zina za Thupi"Pakuti mfumu ya ku Babulo aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mibvi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi ciwindi." Ezekieli 21:21
Kucita Matsenga Pogwiritsa
Ntchito NdodoAnthu anga afunsira ku mtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wacigololo wawalakwitsa, ndipo acita cigololo kucokera Mulungu wao. Hoseya 4:12
Kulangidwa Chifukwa Chochita
MatsengaMomwemo Sauli anafa, cifukwa ca kulakwa kwace analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunga; ndiponso cifukwa ca kufunsira wobwebweta, kufunsirako, osafunsira kwa Yehova.... 1 Mbiri 10:13, 14
"Ndipo alauli adzacita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru;...pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe." Mika 3:7
M'MENE A KARONGA A DZIKO LAPANSI AMACHITIRA 16
Anthu Akunja Amatsata
Zizindikiro Za M'thambo Kapena NyenyeziAtero Yehova, "Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo." Yeremiya 10:2
Musamakhulupilire malemba kapena zinthu zina kuti mukhale ndi mwayi kapenanso kugonjera nyimbo ndi zithunzi zoipa. "Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga...." (Masalmo 101:3.) Siyani kunyada, chinyengo, ndipo chipembedzo choipa.
"Muli ndi tsoka,...inu anthu achiphamaso!...amene amaoneka okongola kunja, koma chonsecho, m'kati mwake ngodzaza ndi...zonyansa zina zonse." Mateo 23:27
Kudzipha Kumachokera
Kwa SatanaMusakhulupilire bodza la Satana, kapena mizimu yoipa loti akuuzeni ngati kudzipha nokha mudzasiyana ndi mavuto ndikukhala opanda chikumbumtima! "Usaphe." (Eksodo 20:13)
Ndi Kristu Yekha Amatimasula
Kuchokera Ku MachimoYehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Ndipo wakhala cipulumutso canga.... Eksodo 15:2
CHENJERANI NDI MAU A SATANA 17
Kupyolera Mwa Aneneri
OnyengaNdipo Yehova anati kwa ine, "Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao." Yeremiya 14:14
Kupyolera Mkulankhula Ndi
Anthu AkufaMotsogozedwa ndi Mulungu, Mfumu Davide ananena za mwana wake wamwamuna, "Koma tsopano wafa,...iye sadzabweranso kwa ine." 2 Samueli 12:23
Osalankhulana ndi mizimu yoipa, koma kuilamula mizimuyo m'dzina la Kristu kuti ichoke. Osakhulupilira kuombeza maula kapena kuombezera ulendo ndi ufiti uliwonse. "...Wopulumutsa ndiye Yehova" (Miyambo 21:31.)
Tayani Mafano, Kapena Mabuku
Onena Za UsatanaAmbiri amene analikuchita matsenga, anasonkhanitsa mabuku awo naëatentha pamaso pa anthu onse. Pamene anaonkhetsa mtengo wake wa mabukuwo, anapeza kuti unakwanira ngati makwacha masauzande asanu. Motero mawu a Mulungu ananka nafalikirafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu. Ntchito 19:19, 20
(Werengani Genesis 35:2-5.)
KRISTU ANALENGA UKWATI SATANA ALEKANITSA UKWATI 18
Ndipo nthitiyo anaicotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. Cifukwa cotero mwamuna adzasiya atate wace ndi amace nadzadziphatika kwa mkazi wace: ndipo adzakhala thupi limodzi. Genesis 2:22, 24
Ukwati muziulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi awo azikhala okhulupirika, pakuti adama ndi achigololo Mulungu adzaëalanga. Aheberi 13:4
Lamulo langa (osatinso langa, koma la Ambuye) kwa anthu a m'banja ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. Koma ngati amleka, akhale wosakwatiëanso, kapena ayanjanenso ndi mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake. 1 Akorinto 7:10, 11
(Onani Aroma 7:2; Marko 10:9.)
Munthu amene amachimwa, ngwa Satana, pakuti Satana ngochimwa kuyambira pachiyambi.... 1 Yohane 3:8
Inu Mumakhala Munthu Wa
Yemwe MukumumveraMudziëa kuti mukadzipereka kukhala akapolo a munthu wina ndi kumamumvera, pamenepo ndinu akapolo a munthuyo amene mumamumvera.... Aroma 6:16
KUCHITA CIGOLOLO NDI CHIWEREWERE NDI KUGALUKIRA MULUNGU 19
"Usacite cigololo." Eksodo 20:14
Chimene Mulungu afuna ndi chakuti mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipeëa dama. 1 Atesalonika 4:3
"Munthu akacita cigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wacita cigololo ndi mkazi wa mnansi wace, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.'' Levitiko 20:10
Ndi izi: dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,...kuti iwo amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu. Agalatia 5:19, 21
Kuchimwira Thupi Lanu
...Thupi la munthu si lochitira dama, koma nla Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo eni ake thupilo. Kodi simudziëa kuti matupi anu ndi ziëalo za Kristu?...Thaëani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu achita siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. 1 Akorinto 6:13, 15, 18
Anakubala Athandize Ana Awo
Kuti Anawo Asacite CigololoUsamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumcititsa cigololo; lingadzale ndi cigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zocititsa manyazi. Levitiko 19:29
IMFA YA KRISTU INAPAMBANA SATANA 20
Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa ali mwa Kristu. 1 Akorinto 15:22
Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe anasanduka munthu wonga iwowo. Iye anachita zimenezi kuti ndi imfa yake awononge Satana, amene anali nayo mphamvu paimfa. Anachitanso zimenezi kuti amasule iwo amene pamoyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. Aheberi 2:14, 15
...Mwana wa Mulungu anaoneka ndi cholinga chakuti awononge zochita za Satana. 1 Yohane 3:8
Tikakhala Mwa Kristu Mzimu
Wathu SudzafaIye anatipulumutsa, ndipo anatiitana kuti tikhale anthu ake. Sanachite zimenezi chifukwa kuti ife tinachita zabwino ayi, koma chifukwa Iye mwini anazikonzeratu motere, ndiponso chifukwa mwa Kristu Yesu anatikomera mtima nthaëi isanayambe. Koma tsopano, Mulungu watiululira zimenezi mwa kubwera kwa Mpulumutsi wathu, Kristu Yesu. Kristuyo anathetsa mphamvu ya imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsera poyera moyo umene sungafe konse. 2 Timoteo 1:9, 10
AKRISTU AMAPAMBANA SATANA 21
...Mdani wanu Satana amayendayenda ngati mkango wobangula namafunafuna woti amudye. Limbanani naye mutakhazikika m'chikhulupiriro.... 1 Petro 5:8, 9
Bvalani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika pakukana machenjerero a Satana....mutabvala choona ngati lamba m'chiuno mwanu. Bvalani chilungamo ngati malaya achitsulo otchinjirizira pachifuwa chanu, ndipo kukonzeka kwanu kulalika Uthenga Wabwino wa mtendere kukhale ngati nsapato zanu. Nthaëi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chisyango chanu, chimene mudzatha kuzimitsira mibvi yonse yoyaka moto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mawu a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani....Panthaëi iliyonse pempherani...ndi Mzimu Woyera. Aefeso 6:11-18
Mugonjere Mulungu tsono. Mumkane Satana, ndipo adzakuthaëani. Yakobo 4:7
...[Kristu] amene ali mwa inu, ngopambana Satana amene ali mwa anthu ongokonda zapansi pano. 1 Yohane 4:4
Chifukwa chiyani Satana amathawa? Cifukwa Kristu ali mkati mwanu!
ULAMULIRO WA KRISTU 22
Iye Ndiye Mau A Mulungu
...Mulungu... koma pamasiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi Iyeyu Mulungu analenga zolengedwa zonse, ndipo anamuika kuti akhale mwini zonse. Aheberi 1:1, 2
Anthu anadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa pophunzitsa analikusiyana ndi aphunzitsi a Malamulo a Mose, popeza kuti Iye ankaphunzitsa ndi ulamuliro.Marko 1:22
Chifukwa analikuëaphunzitsa monga mwini mphamvu, osati monga m'mene aphunzitsi a Malamulo ankachitira. Mateo 7:29
"Ndipo anapatsa Mwanayo mphamvu yoweruzira milandu, chifukwa ndiye Mwana wa Munthu." Yohane 5:27
Yesu anapita Kumwamba, ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye. 1 Petro 3:22
Pakuti Kristu anamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo. Aroma 14:9
Yesu anadza pafupi naëauza kuti, "Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndiponso pansi pano." Mateo 28:18
KRISTU AMALANKHULA NACHITA ULAMULIRO 23
Yesu anadzuka, ndipo analetsa mphepoyo, nalamula nyanja kuti, "Tonthola! Khala bata!" Mphepo ija inalekadi, ndipo kunagwa bata lalikulu. Marko 4:39
Iye Anachiza Ndi
Ulamuliro Wake"Ndikuonetsani kuti Mwana wa Munthu ali ndi mphamvu zokhululukira machimo pansi pano." Apo anauza munthu wa ziëalo zakufa uja kuti, "Ndilikukulamula, dzuka, tenga tchika lako, uzipita kwanu." Munthu uja anadzukadi, natenga tchika lija ndi kutuluka, onse aja akuona. Onsewo anazizwa kwambiri, natamanda Mulungu.... Marko 2:10-12
Apo chiëanda chinkamuipitsa chija chinamgwedeza kwamphamvu, ndipo chinakuëa kwambiri, ndi kutuluka mwa iye. Anthu onse anadabwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, "Kodi zimenezi nzotani? Zimenezitu ndi ziphunzitso zatsopano. Ngakhale ziëanda zonyansa zomwe akuzilamula ndi mphamvu, ndipo zikumumveradi." Marko 1:26, 27
Tsono anafika pafupi nakhudza chithatha. Anthu amene analikunyamula malirowo anaima, ndipo Yesu anati, "Mnyamata iwe, ndikukuuza kuti, Uka." Pamenepo wakufayo anakhala tsonga nayamba kulankhula, ndipo Yesu anampereka kwa mayi wake. Luka 7:14, 15
KRISTU AMAPATSA OTSATIRA AKE MPHAMVU NDI ULAMULIRO OPAMBANA MPHAMVU YA MDANI 24
"Ndilikukupatsani mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndiponso kuti muzipambana mphamvu zonse za mdaniyo. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni." Luka 10:19
Yesu anaitana ophunzira ake khumi ndi aëiri aja naëapatsa mphamvu ndi ulamuliro paziëanda zonse, ndiponso zochiritsira nthenda. Luka 9:1
..."Zoonadi, ngati mukhulupirira Mulungu, mungathe kulamula phiri ili kuti, `Nyamuka, kadziponye m'nyanja!' Mutanenadi ndi mtima wosapeneka, koma ndi chikhulupiriro kuti chimene mukunenacho chichitikadi, chidzachitikadi." Marko 11:22, 23
Yesu anati, "Bwanji mukuti, `Ngati mungathe'? Zinthu zonse nzotheka kwa yemwe ali ndi chikhulupiriro." Marko 9:23
Ndiponso mudziëe mphamvu yake yaikulukulu imene ilikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa. Aefeso 1:19
Ndingathe kuchita zonse chifukwa Kristu amandipatsa mphamvu. Afilipi 4:13
TITUIUTSA BWANJI MIZIMU YOIPA? 25
Idzudzuleni. Ilamuleni Kuti
Ituluke M'dzina La YesuChiëandacho chinanena mawu ameneëa chifukwa Yesu nkuti atachilamula kuti, "Chiëanda chonyansawe, tuluka mwa munthuyu!" Yesu anamfunsa munthuyo kuti, "Dzina lako ndani?" Iye nayankha kuti, "Dzina langa ndine `Chikhamu', chifukwa tilipo ambiri." ...Tsono ziëanda zonyansazo zinatuluka mwa munthu uja, ndipo zinakaloëa m'nkhumbazo.... Marko 5:8, 9, 13
...Yesu...analamula chiëanda chonyansacho kuti. "Iwe chiëanda choletsa kulankhula ndi kumva, ndikukulamula kuti utuluke mwa mwanayu, ndipo usadzaloëenso mwa iye." Chiëandacho chinapfuula ndipo chinamzunguza mwaphamvu mwana uja, kenaka nkutuluka. Mwanayo anangokhala ngati kuti wafa, mpaka ambiri nkumati, "Watsirizika!" Koma Yesu anamgwira dzanja namdzutsa, ndipo mwanayo anaimirira. ..."Chiëanda cha mtundu umenewu, mapemphero okha ndiwo angachitulutse." Marko 9:25-27, 29
...Paulo...anapotoloka nauza chiëanda chija kuti, "Ndilikukulamula m'dzina la Yesu Kristu kuti utuluke mwa iye." Ndipo chinatulukadi nthaëi yomweyo. Ntchito 16:18
DZINA LALIKULU LA YESU KRISTU 26, 27
Chifukwa cha chimenechi Mulungu anamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Anachita zimenezi kuti zinthu zonse za Kumwamba, za pansi pano, ndiponso za pansi padziko, zidzagwade pansi ndi kuchitira ulemu dzina la Yesu. Afilipi 2:9, 10
``Chilichonse chomwe mudzachipemphe m'dzina langa ndidzachita, kuti Atate akalemekezedwe chifukwa cha Mwana.'' Yohane 14:13
Banja langa ndi ine, tinapita ku Africa kukagwira ntchito ya Kristu. Ndinadzuka usiku wina nditamva mzimu woipa uli pamwamba panga. Ndinavutika, naopa kwambiri, koma ndinalira, ``Yesu, ndithandizeni!'' Panthawi yomweyo mzimuwo unacoka kusabweranso. M'dzina la Yesu Kristu mulindi mphamvu yodabwitsa kupambana Satana ndi mizimu yoipa yonse. Itanani pa dzina la Yesu Kristu kukupulumutsani inu (Aroma 10:13).
Mkazi wina anandiuza ine ndi mkazi wanga kuti pamene iye anali mtsikana, napita kusukulu, mwamuna wina anamvutitsa nayesa kumupha. Mkaziyo anapfuula m'dzina la Yesu Kristu. Nthawi yomweyo mwamunayo sanakhoza kuchita kanthu kali konse, naleka kumvutitsa. Ndipo sanayesanso kuvutitsa mtsikanayo.
Mkazi wina anandiuza ine ndi mkazi wanga kuti pamene anali wamng'ono analoleza gulu la anthu a maula kuti alowe m'nyumba mwake. Atatero mizimu yoipayo inayamba kusuntha mipando ndi matebulo m'nyumbamo. Atavutika choncho, anatulutsa anthuwo m'dzina la Yesu, nadzipeleka kwathunthu kwa Yesu Kristu.
Musamumvere chisoni Satana kapena mizimu yoipa. Cholinga chake ndi chakuti inu mukhale mbali yake osati ya Mulungu. Mkristu wachikulire yemwe anali wofoka ndi wosokonezeka m'maganizo anandiuza zomwe Santana ankamuuza. Ndinanena kuti Satana ndi mbuye wabodza ndipo sitiyenera kumumvera. Ndinamudzudzula mudzina la Yesu. Munthuyo anati, "Ndakondwera kuti munabwera usiku uno". Anaoneka kuti anali ndi mtendere sabata zisanu asanamwalire. Watson Goodman
KUSIYANITSA KRISTU NDI SATANA 28
Kristu Ndiye Mulungu Mlengi
Mwa Iye Mulungu analenga zonse za kuthambo ndiponso za pansi pano, zooneka ndiponso zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndiponso amphamvu. Mulungu analenga zonse mwa Iye, ndipo zonse zimalinga kwa lye. Akolose 1:16
Kristu Amapatsa Kuwala
Ndi Mtendere"Kuëalako kudzaunikira onse okhala mumdima ndi mumthunzi wa imfa, ndipo kudzatitsogolera panjira yamtendere." Luka 1:79
Ambuye mwini, amene amapatsa mtendere, akupatseni mtendere nthaëi zonse.... 2 Atesalonika 3:16
Mizimu Yoipa Ndi Satana
Amaononga"Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga...." Yohane 10:10
"...Koma muli ndi tsoka, dziko lapansi...pakuti Satana watsikira kwa inu. Ali wokalipa kwambiri...." Chibvumbulutso 12:12
Satana Amapatsa Mdima
Ndi MasautsoNjira ya oipa ikunga mdima.... Miyambo 4:19
"...Munthu wachuma uja nayenso anamwalira, naikidwa m'manda. Pamene analikuzunzika ku Malo a anthu akufa, anayang'ana kumwamba...." Luka 16:22, 23
KUSIYANITSA KRISTU NDI SATANA 29, 30
Kristu Ndiye Choonadi
Mawuwo anasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Tinaona ulemerero wake umene Iye, Mwana mmodzi yekha wa Atate, anaulandira kwa Atate ake. Anali wokoma mtima ndi woona kotheratu...."Ngati musunga mawu anga nthaëi zonse....Mudzadziëa choona, ndipo choonacho chidzakupatsani ufulu." Yohane 1:14; 8:31, 32
Kristu Ndi Wodzala
Ndi ChikondiTazindikira chikondi tsopano pakuona kuti Kristu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha anzathu. 1 Yohane 3:16
Satana Ndiye tate Wabodza
"Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mulikufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iyeyu kuyambira pachiyambi ndithu amapha anthu. Sali pazoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndilo khalidwe lake, pakuti iye ngwabodza, ndiyenso tate wa mabodza onse." Yohane 8:44
Satana Amabweretsa Chidani
"Ngati anthu ongokonda zapansi pano adana nanu, kumbukirani kuti anadana ndi Ine asanadane nanu." Yohane 15:18
Kristu Amasambitsa Mtima
Koma tikamayenda m'kuëala,...pamenepo tilikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatisambitsa ndi kutichotsera tchimo lililonse. 1 Yohane 1:7
Kristu Amapulumutsa
Kuchokera Ku Machimo...Makamaka adzatipulumutsanso ndithu kumkwiyo wa Mulungu. Aroma 5:9
Kristu Amapatsa Moyo
Wosatha"Ndipo moyo wosathawo ndi wakuti akudziëeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziëenso Yesu Kristu amene munamtuma." Yohane 17:3
Satana Amaipitsa Mtima
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo, Chimene munthu amene angodzikhulupirira yekha adzakolole, ndi imfa.... Agalatia 6:7, 8
Satana Amanyengelera Anthu
Kuti AchimweMunthu amene amachimwa, ngwa Satana.... 1 Yohane 3:8
Satana Amatsogolera Anthu
Ku Imfa Yosatha"...Namsongole uja ndiwo anthu a Woipa uja....anazulira namsongole uja ndi kumtentha pamoto...." Mateo 13:38-40
SATANA NDI ULAMULIRO WA DZIKO LONSE LAPANSI 31
Satana Ndiye Mfumu Ya Dziko Lapansi
"Sindilankhula nanunso zambiri tsopano ayi, pakuti Satana, mfumu ya anthu oipa a dziko lapansi, alikudza. Iyeyo alibe ulamuliro pa Ine." Yohane 14:30
Ngati zina sizikuyenda Bwino,
Mumuzenge Iye MulanduNzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma nza pansi pano, za anthu chabe, ndiponso nzochokera kuziëanda. Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse. Yakobo 3:15, 16
Khalani Okhulupirika Kwa
Kristu Kufikira ImfaAnthu aja alikumponya miyala Stefano, Stefanoyo anapemphera kuti, "Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.'' Ndipo anagwada pansi napfuula kolimba kuti, "Ambuye, musaëaëerengere tchimo ili." Atanena mawu ameneëa, anamwalira. Ntchito 7:59, 60
Za kuenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikitsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse.... Yesaya 9:7
WOKANA KRISTU MFUMU YA DZIKO IDZABWERA 32
Abale, kunena za kubweranso kwa Ambuyathu Yesu Kristu, ndiponso za kusonkhana kwathu pamodzi kwa Iye....Musalole kuti munthu aliyense akupusitseni mwa njira iliyonse. Pakuti lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika Chipatuko chachikulu, ndiponso kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, amene ayenera kutayika. Ndiye mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu. Ndipo pambuyo pake Munthu Woipitsitsa uja adzaululuka. Ambuye Yesu adzamupha ndi mpweya wotuluka m'kamwa mwake, nadzamuwononga ndi maonekedwe ake aulemerero pamene adzabwere. Munthu Woipitsitsa uja adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzachita zamphamvu zosiyanasiyana, ndiponso zizindikiro ndi zozizwitsa zonyenga. 2 Atesalonika 2:1, 3, 4, 8, 9
...Chinjoka chija chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu, ndiponso ulamuliro waukulu....Chinapatsidwanso mphamvu yolamulira pfuko lililonse, anthu a mtundu uliwonse, ndiponso a chinenero chilichonse. Chibvumbulutso 13:2, 7
WOKANA KRISTU ADZACHITA NKHONDO NDI OYERA MTIMA 33
Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi cilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lace mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu. Danieli 7:25
...Chinapatsidwanso mphamvu yolamulira miyezi 42. Tsono chinayamba kunena mawu onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndiponso onse okhala Kumwamba. Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi anthu a Mulungu ndi kuëagonjetsa. Chinapatsidwanso mphamvu yolamulira pfuko lililonse, anthu a mtundu uliwonse, ndiponso a chinenero chilichonse. Anthu onse okhala padziko lapansi adzachipembedza. Ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silinalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa amene anaphedwa. Ngati wina ali ndi makutu, amve. Chibvumbulutso 13:5-9
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Pakuti Mulungu anakuitanira zimenezi, ndipo unabvomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri. 1 Timoteo 6:12
OSAPEMBEDZA CHIFANIZO CHA OKANA KRISTU 34
Mtsogoleri wa mpingo pa
dziko lonse lapansiChinalikunyenganso anthu okhala padziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chinaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinauza anthu okhala padziko lapansi kuti apange fano lolemekezera nalo chilombo chija chimene chinalasidwa ndi lupanga, komabe chinakhala ndi moyo. Chinaloledwa kuuzira mpweya wopatsa moyo mufano lija la chilombo choyamba chija, kuti mpaka lilankhule, ndi kuphetsa aliyense wosalipembedza. Chilombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake....Ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aëiri anaëaponyera m'nyanja yamoto.... Chibvumbulutso 13:14, 15; 19:20
Anthu A Mulungu Amakana
milungu Yina"...Nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudalimikalo." Danieli 3:17, 18
WOKANA KRISTU: GONJANI KAPENA MUMVE NJALA 35
Chinakakamiza anthu onse, ang'ono ndi akulu, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti alembedwe chizindikiro padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo. Chinachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi. Chizindikiro chake ndicho dzina la chilombo choyamba chija, kapena ëerengo la dzina lake....Yemwe ali ndi nzeru aëerengere ëerengo la chilombolo, pakuti ëerengolo ndi la munthu. êerengo lake ndi 666. Chibvumbulutso 13:16-18
Tsiku Labwino Likubwera Kwa
Opulumutsidwa..."Ameneëa ndi amene anali m'masautso akulu aja. Anachapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa. Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Sadzaëambikanso ndi dzuëa kapena kusauka ndi kutentha. Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wawo, ndipo adzaëatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Mulungu adzaëapukuta misozi yawo yonse m'maso mwawo." Chibvumbulutso 7:14, 16-17
Kulowa kumwamba ndi njala nkwabwino koposa kulowa ku gehena utakhuta!
ONSE OPEMBEDZA OKANA KRISTU ADZAONONGEDWA, KAPENANSO OKHALA NDI CHIZINDIKIRO PATHUPI PAO KUTI ATHE KUGULA KAPENA KUGULITSA 36
Kenaka panafikanso mngelo wina wachitatu, wotsatana ndi aëiri ena aja. Mokweza mawu iye anati, "Aliyense wopembedza chilombo chija ndiponso fano lake, ndi kulandira chizindikiro chija pamphumi pake kapena padzanja lake, ndiye amene adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyoyo adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzika ndi moto ndiponso ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitika pamaso pa angelo a Mulungu, ndiponso pamaso pa Mwanawankhosa uja....Iwo amene anapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene analandira chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku." Pambuyo pake ndinamva mawu ochokera Kumwamba. Anati, "Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano afa ali okhulupirira Ambuye."... Chibvumbulutso 14:9-11, 13
CHIGONJETSO CAKUPAMBANA LEMBA NDI FANO LA SATANA USANAFIKE MKWIYO WA MULUNGU PA DZIKO LAPANSI 37
...Panali angelo asanu ndi aëiri okhala nayo miliri isanu ndi iëiri. Miliriyo njotsiriza, pakuti ukali wa Mulungu uthera paimeneyi. Kenaka ndinaona ngati nyanja yagalasi losakaniza ndi moto. Ndinaonanso iwo amene anapambana chilombo chija, fano lake lija, ndiponso ëerengo la dzina lake. Anaimirira pamphepete pa nyanja yagalasi ija, ali ndi azeze amene Mulungu anaëapatsa. Pambuyo pake ndinamva mawu amphamvu ochokera m'Malo Opatulika muja. Anauza angelo asanu ndi aëiri aja kuti, "Pitani, katsanuleni padziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mbale zisanu ndi ziëiri zija." Chibvumbulutso 15:1-2; 16:1
...Ndinaonanso mizimu ya anthu amene anaëadula pakhosi chifukwa cha kuchitira Yesu umboni, ndiponso chifukwa cha kulalika mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chilombo chija kapena fano lake lija, ndipo anakana kulembedwa chizindikiro chija pamphumi pawo kapena padzanja. Anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Kristu zaka sauzande. Chibvumbulutso 20:4
HARMAGEDO, NKHONDO YOMWE KRISTU AMALETSA 38
Ziwanda Zisonkhanitsira Mafumu Kuti Amenyane Nkhondo
Mizimuyo nja ziëanda, ndipo imachita zozizwitsa. Imapita kwa mafumu a padziko lapansi kukaëamema, kuti adzabwere kunkhondo ya patsiku lalikulu lija la Mulungu Wamphamvuzonse. Pamenepo mizimu ija inasonhanitsa mafumu aja kumalo amene pa Chiyuda amatchedwa "Harmagedo." Chibvumbulutso 16:14, 16
Kristu Amasula Dziko Lake
ndi Anthu Ake Osankhika, Aisrayeli"Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu....Pamenepo Yehova adzaturuka, nadzacita nkhondo ndi amitundu aja, monga anacitira nkhondo tsiku lakudumana." Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali ciriri pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuala m'pfunkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao. Zekariya 12:3; 14:3, 12
...Popeza kuti Mulungu amatithandiza, kodi angatsutsane nafe ndani?
Aroma 8:31KRISTU ADZAPAMBANA KUKHALA MFUMU YOLAMULA DZIKO LONSE LAPANSI 39
M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzagonjetsere mitundu ya anthu. Adzaëalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'choponderamo mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Wamphamvuzonse. Pachobvala chake, ndiponso pantchafu yake panalembedwa dzina loti, "Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse." Chibvumbulutso 19:15, 16
"...Ndipo adzalamula mpaka muyaya." Chibvumbulutso 11:15
Wokana Kristu Alamulira
Zaka Zochepa. Kristu Alamulira Zaka Zikwi....Koma adzakhala ansembe a Mulungu ndiponso a Yesu Kristu, ndipo adzalamulira pamodzi naye zaka sauzande. Chibvumbulutso 20:6
"Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka ku nthawi zonse...." Danieli 2:44
Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; Nadzalemekeza dzina lanu. Masalmo 86:9
MULUNGU AMAMUPAMBANA NKHONDO SATANA 40
Chinjoka chachikulu chija chinaponyedwa kunja. Ichochi ndicho njoka yakale ija yotchedwa "Mdyerekezi" ndiponso "Satana", wonyenga dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa padziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse. Pamenepo ndinamva mawu amphamvu Kumwamba alikunena kuti, "Tsopano Mulungu watipulumutsa. Tsopano Mulungu wathu waonetsa mphamvu yake ndiponso ufumu wake. Tsopano Mfumu imene Iye anaidzoza yaonetsa ulamuliro wake. Pakuti woneneza abale athu uja waponyedwa kunja, iye amene ankaëaneneza kwa Mulungu wathu usana ndi usiku." Chibvumbulutso 12:7-10
Zida Zopambanira Nkhondoyi
"Abale athuwo anamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mawu a Uthenga umene ankauchitira umboni. Iwo anadzipereka kotheratu, kotero kuti sanaope ngakhale kufa." Chibvumbulutso 12:11
Pa Chimaliziro Cha Dziko,
Satana Adzaponyedwa Ku Nyanja Yotentha Ndi MotoPamenepo Satana amene anaëanyenga, anaponyedwa m'nyanja yamoto woyaka ndi miyala ya sulufure....M'menemo adzazunzidwa kwamuyaya usana ndi usiku. Chibvumbulutso 20:10
UFUMU WAMUYAYA NDI WA NDANI? 41
Kristu Ambuye Alamulira Ku
Nthawi Za NthawiUkulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi cifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. 1 Mbiri 29:11
Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa ali mwa Kristu. Koma aliyense adzauka panthaëi yake: woyambirira ndiye Kristu, ndipo pambuyo pake, pamene Kristuyo adzabwera, iwonso amene ali ake adzauka. Pamenepo chimalizo chidzafika. Kristu adzathetsa oweruza onse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse, nadzapereka ufumu wonse kwa Mulungu Atate. Pakuti Kristu ayenera kukhala Mfumu, mpaka Mulungu atagonjetsa adani ake onse. Mdani wotsiriza amene Mulungu adzamthetsa mphamvu, ndiye imfa. 1 Akorinto 15:22-26
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiëiri analiza lipenga lake, ndipo kunamveka mawu amphamvu Kumwamba. Mawuwo anati, "Tsopano mphamvu yolamulira dziko lapansi ili m'manja mwa Ambuyathu ndi mwa Mfumu imene anaidzoza, ndipo adzalamula mpaka muyaya." Chibvumbulutso 11:15
SATANA NDI MIZIMU YOIPA NDI ADANI ANU 42
Satana Amaononga Thupi Ndi
Mzimu Pamene Anthu Achita Zoipa Zosiyanasiyana...Amuna...akumakhumbana amuna okhaokha....anadziitanira chilango chimene chinaëayenera chifukwa cha ntchito zawo.... Aroma 1:27
Ziripo zinthu...Mulungu azida;...manja akupha anthu osacimwa. Miyambo 6:16, 17
"Tsono chimapita ndi kukatenga ziëanda zina zisanu ndi ziëiri zoipa koposa ichocho, ndipo chimaloëa ndi kukhala m'menemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba...." Mateo 12:45
Si zododometsa zimenezi ayi, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. 2 Akorinto 11:14
Funafunani Mulungu Wamoyo Yekha. Osayitana milungu yina yochita zoipa zosiyanasiyana.
Satana, wogalukira Mulungu, amachita zonsezi. Amagwiritsa ntchito anthu, mabukhu, zinthu zowoneka ndi maso, zipembedzo zonama. Zochita zachet poyamba zimaoneka zodabwitsa ndi zothandiza, koma zimapangitsa ukapolo. Kristu yekha angakumasuleni.
Osadzipeleka ku ulamuliro uli wonse womwe si wa
Mzimu Woyera Wa Mulungu. Mukhulupilire Bukhu Lopatulika ndi Yesu Kristu.
(Onani Cibvumbulutso 19:13.)
AMBIRI ADZABWERA NADZASOCHERETSA AMBIRI 43
Ciphunzitso chiri chonse chomwe chimakuchotsani ku cikhulukiro, kusambitsidwa, ndi chiombolo kupyolera mu mwazi wa Kristu ndi chonyenga.
Yesu anaëayankha kuti, "Chenjerani kuti wina aliyense asadzakunyengeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa nadzanena kuti, `Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine', ndipo adzasokeretsa anthu ambiri. Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeretsa anthu ambiri." Mateo 24:4, 5, 11
Ndakhala ndilikukuuzani kaëirikaëiri, ndipo tsopano ndilikubwerezanso kukuuzani molira misozi, kuti alipo ambiri amene mayendedwe awo amatsimikizira kuti ndiwo adani a mtanda wa Kristu. Potsiriza adzawonongeka. Mimba yawo ndiyo mulungu wawo.... Afilipi 3:18, 19
Mwazi Wopambana Wa Kristu
Umawombola...Sanakuwomboleni ndi ndalama zimene zimawonongeka, koma anakuwombolani ndi imfa yamtengo wapatali ya Kristu, amene anakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema. Mwa iye mumakhulupirira Mulungu.... 1 Petro 1:18, 19, 21
MUNTHU WOSAUKA INE 44
Wolamulidwa Ndi Chikhalidwe
Cha UchimoPakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse ziri ngati cobvala codetsedwa.... Yesaya 64:6
Mkwiyo Pa Mzimu Wa
KusamveraPanthaëi imeneyo, mayendedwe anu analikulingana ndi mayendedwe a anthu ongokonda zapansi pano, ndipo munalikumvera mkulu wa aulamuliro mumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ulikugwira ntchito tsopano pakati pa anthu osamvera Mulungu. Nthaëi ija tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, ndipo tinalikutsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu analikufuna.... Aefeso 2:2, 3
Satana Ndiye mbuye Wa
OsapulumutsidwaKoma ngati Uthenga Wabwino umene timalalika uli wophimbikabe, ngophimbika kwa okhawo amene alikutayika. Iwoëa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, anachititsa khungu maganizo awo, kuopa kuti angaone kuëala kwa Uthenga Wabwino. Kuëalako kumaonetsa ulemerero wa Kristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka. 2 Akorinto 4:3, 4
ANTHU OSAPULUMUTSIDWA NDI A SATANA 45
"Munda uja ndiwo dziko lapansi. Mbewu zabwino zija ndiwo anthu amene ali a Ufumu wa Mulungu. Namsongole uja ndiwo anthu a Woipa uja." Mateo 13:38
"Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mulikufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka...." Yohane 8:44
Mwa Adamu, Ndife Ogalukira
Mulungu"Munthu amene sabvomerezana ndi Ine, amatsutsana nane. Ndipo amene sasonkhanitsa pamodzi ndi Ine, ameneyo amamwaza." Mateo 12:30
Ichi Ndi Chifukwa Chake
Tiyenera Kubadwanso Mwa MzimuNgati munthu ali mwa Kristu, ngolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, ndipo zimene zilipo nzatsopano. 2 Akorinto 5:17
Dzipelekeni Kwa Ambuye Yesu
Kristu Tsopano...Mvetsani, yino ndiyo nthaëi yabwino imene Mulungu alikukomera anthu mtima. Lero ndilo tsiku la chipulumutso. 2 Akorinto 6:2
Koma tikamabvomera machimo athu, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse. 1 Yohane 1:9
CHIGONJETSO CHOSATHA MWA KRISTU 46
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Kristu? Masautso kodi, kapena zoëaëa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiëa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Koma pazonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene anatikonda. Aroma 8:35, 37
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera nacho dziko lapansilo, ndicho chikhulupiriro chathu. 1 Yohane 5:4
Amapeleka Mphotho Kwa
Onse Opambana"Amene ali nawo makutu, amve zimene Mzimu Woyera alikuuza mipingo. Amene adzapambane, ndidzampatsa chakudya cha Kumwamba, chosaoneka ndi maso. Ndidzampatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziëa iye yekha, osati wina aliyense." Chibvumbulutso 2:17
"Amene adzapambane ndi kuchita mpaka potsiriza zimene ndamlamula, ndidzampatsa ulamuliro pamitundu yonse ya anthu." Chibvumbulutso 2:26
Muli wofunika kwa Mulungu.
Chifukwa cha Kalvari.MUDZISANKHIRE AMENE MUDZAMTUMIKIRA NTHAWI YOSATHA 47
Kuoneka Ndi Kristu Mu
UlemeleroMunaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, tsono ikani mtima pazinthu za Kumwamba, kumene Kristu alikukhala kudzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za Kumwamba, osati za pansi pano. Kristu ndiye moyo wanu, ndipo pamene Iye adzaonekere, inunso mudzaonekera muulemerero pamodzi naye. Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amakwiyira anthu osamumvera. Akolose 3:1, 2, 4, 6
Kapena Kutembereredwa Ndi
Satana Kwamuyaya"Pamenepo idzauzanso a kudzanja lake lamanzere aja kuti, `Chokani, inu anthu otembereredwa. Pitani kumoto wosatha umene Mulungu anaukonzera Satana ndi angelo ake.'" Mateo 25:41
Oipawo adzabwerera kumanda, Inde amitundu onse akuiwala Mulungu. Masalmo 9:17
"Ndipo ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino koposa kuti ukaloëe kumoyo wosatha uli woduka dzanja, kupambana kuti ukaloëe uli ndi manja onse aëiri ku Gehena, kumoto wosazimika." Marko 9:43
UFUMU WA MULUNGU NDI WANU 48
Mudzichepetse Nokha
Apo Yesu anaitana mwana namuimiritsa pakati pawo, ndi kuëauza kuti, "Zoonadi ndikukuuzani kuti mukapanda kusinthika ndi kukhala ngati ana, simudzaloëa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Nchifukwa chake munthu amene adzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba." Mateo 18:2-4
Lapani Machimo
Zimenezi zinachitikadi pamene Yohane Mbatizi anafika kuchipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, "Lapani, batizidwani, ndipo Mulungu adzakhululukira machimo anu." Yohane uja ataponyedwa m'ndende, Yesu anapita ku Galilea alikulalika Uthenga Wabwino wochokera kwa Mulungu. Ankati, "Nthaëi yakwana, Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano. Lapani ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu." Marko 1:4, 14, 15
"Iyayi, koma ngati simulapa, inunso mudzawonongedwa monga iwo aja." Luka 13:3
"Nchifukwa chake lapani, bwererani kwa
Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu."
Ntchito
3:19
(Mau akupitilira pa tsamba linalo.)
LANDIRANI KRISTU MONGA MPULUMUTSI WANU LERO!
Mudzipereke Nokha Kwa
Yesu KristuPereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzacicita. Masalmo 37:5
"Pakuti Mulungu anakonda anthu a padziko lonse lapansi kwambiri. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe anampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha." Yohane 3:16
..."Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'banja mwako." Ntchito 16:31
Komabe anthu onse amene anamlandira ndi kumkhulupirira, Iye anaëapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu. Yohane 1:12
Bvomerezani Kristu Poyera
...Ubvomereza pakamwa pako kuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo ngati ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Chifukwa munthu ayenera kukhulupirira ndi mtima wake, kuti Mulungu amlungamitse, ndipo ayenera kubvomereza chikhulupiriro chakecho pakamwa pake, kuti apulumuke. Aroma 10:9-10
Kabukuka kasindikizidwa m'zinenero zambiri kupereka kwaulere kwa anthu a padziko lonse lapansi. Ngati mufuna timabuku tina, lemberani kwa ife m'Chizungu (English).
If you are interested in receiving additional Scripture booklets, write to the publisher in English at the address below or order online:
World Missionary Press, Inc.
P.O. Box 120
New Paris, Indiana 46553-0120 U.S.A.
World Missionary Press Home Page | Go to the Top of This Page