World Missionary Press

Njira Ya kwa Mulungu - Chichewa

Bookmark and Share  

 

 

 

 

 


©1992 by Rose Goodman. Cover art, Edwin B. Wallace. Meryl Esenwein, are above and on pages 10, 12, 14, 16, 27, 29, 39, 41, 42, 44, 46, 47 and 48. Mau onse a Mulungu olembedwa m'kabuku kano alembedwa kuchokera mu Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, 1981, The Bible Societies Central Africa zonsezi zalembedwa muno mwa chilolezo.


MULUNGU ADAPANGA DZIKO LATHU NDI ZAMOYO ZONSE — 1

"Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi." —Genesis 1:1

"Pakuti mwa lye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko." —Akolose 1:16a

"Odalitsika inu a kwa Yehova, Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu." —Masalmo 115:15, 16

Dziko lapansi lidali langwiro pamene Mulungu adalipereka kwa munthu. Werengani kabukuka kuti muone izo zidachitika.


MULUNGU ADATIPANGA IFE — 2

Ndipo anati Mulungu, "Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire [ulamuliro] pa nsomba za m'nyanja....ndi pa dziko lonse lapansi." —Genesis 1:26a


MUNTHU ANAKHALA WAMOYO — 3

"Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo*." —Genesis 2:7

"Yehova Mulungu ndipo anati, `Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.' Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikuru, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake: ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu." —Genesis 2:18, 21, 22

*Munthu Wamoyo atanthauza kuti tidzakhala muyaya kwinakwake.


ADAMU NDI HAVA SADAMVERE MULUNGU — 4, 5

Tisamvere nkomwe zotiuza Mdierekezi.

Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edene kuti aulime nauyang'anire. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati "Mitengo yonse ya m'munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu." —Genesis 2:15-17

NJOKA, YOTCHEDWANSO SATANA KAPENANSO KUTI MDIEREKEZI, SIDAKHULUPIRIRE MPHAMVU NDI ULAMULIRO WA MULUNGU NDIPO IDANENA BODZA.

Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, "Kufa simudzafai." Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso. —Genesis 3:4, 6


NDIPO ADAMU NDI HAVA SADATHE KUKHALANSO M'MUNDA MUJA — 6

"Yehova Mulungu anamturutsa iye m'munda wa Edene, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye....Nakhazika Makerubi cha kum'mawa kwake...ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo." —Genesis 3:23, 24


LIDALI TSIKU LOMVETSA CHISONI MTUNDU WA ANTHU — 7
ONSE, PAMENE ADAMU NDI HAVA ADACHIMWA

"Monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse...." —Aroma 5:12b

Chinachake Chofunika Kukumbukira 

Munthu aliyense amabadwa ndi uchimo ndipo tsiku lina adzafa popeza imfa idabwera chifukwa cha tchimo. (Werenganinso Aroma 5:12.)


CHIKONZERO CHANZERU CHA MULUNGU CHOTIWOMBOLERA IFE KU UCHIMO CHIDALI KUTUMIZA MWANA WAKE M'MODZI YEKHAYO — 8

"Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti lyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao."      —Mateyu 1:21

Kuti alowe mu mtundu wa anthu (m'dziko lapansi), Mwana wa Mulungu adayenera kubwera ngati mwana wakhanda wa munthu.

"Pakuti mwa lye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi." —Akolose 2:9


YESU NDI MULUNGU MU UMUNTHU — 9

"Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu. Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika [nakhala] pakati pa ife." —Yohane 1:1, 14

Ndipo zonsezi zinakhala..."Onani namwali adzaima, Nadzabala mwana wamwamuna, Ndipo adzamutcha dzina lake, Emanueli;" ndilo losandulika, "Mulungu nafe." —Mateyu 1:22, 23

"Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere." —Yesaya 9:6


YESU KRISTU NSEMBE YATHU YANGWIRO — 10

"Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu." —2 Akorinto 5:21a

"Amene sanachita tchimo." —1 Petro 2:22a

Padalibe nsembe (yopereka) ngakhale yimodzi YANGWIRO yomwe munthu akadapereka kuti yichotse tchimo.

"Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsere machimo." —Ahebri 10:4

Yesu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu. "Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!" —Yohane 1:29b


YESU ANAPEREKA MOYO WAKE KUTI ATIPULUMUTSE — 11, 12

Yesu anakhomedwa ndi misomali pamtanda popeza anthu ankhaza anamuda Iye. Koma imfa yake idali chikonzero chanzeru cha Mulungu. Mwakufuna kwake, Yesu adapereka moyo wake kuti awombole inu ndi ine ku machimo athu.

Yesu anati, "Palibe wina andichotsera [Moyo wanga] uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndiri nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndiri nayo yakuutenganso." —Yohane 10:18a

IFE TAWOMBOLEDWA NDI MWAZI WA MWANAWANKHOSA WA MULUNGU

"Simunaomboledwa [simunapulumutsidwe] ndi zobvunda, golidi ndi siliva,...koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu." —1 Petro 1:18, 19

Palibe nsembe yina yiliyonse yomwe yingachotse tchimo.

"Popeza tinayesedwa olungama [tinayesedwa opanda tchimo] ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo." Aroma 5:9 

"Atate, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu."

Mbava iyi yidakhulupirira Yesu ndipo yidapulumutsidwa .

"Ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso." Luka 23:43b 

Mbava iyi sidakhulupirire Yesu, choncho sidapulumutsidwe .

"Kuti pokhala ife chikhalire ochimwa [osamvera Mulungu], Kristu adatifera ife."     Aroma 5:8b


ONSE AMENE AKHULUPIRIRA MWA MWANA WA MULUNGU ALI NAWO MOYO — 13

"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha."  —Yohane 3:16

"Amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa [kutipititsa] m'ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tiri nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu." —Akolose 1:13, 14

*Kuwomboledwa kutanthauza kuti tagulidwa nkubwerera uko tidachokera.


 "ANAUKA!" — 14

Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, "Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa. Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye." Mateyu 28:5, 6

 


YESU ANAUKA KWA AKUFA — 15

"...ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade." —Chibvumbulutso 1:18

"Popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo." —Yohane 14:19b

Popeza Kristu anagonjetsa imfa ndipo kuti ali ndi zotsekulira za kuimfako, sitiyeneranso kuopa imfa.

"Tsiku lakuopa ine, Ndidzakhulupirira Inu." —Masalmo 56:3

YESU AKHOZA KUKUPULUMUTSANI INU NDIPO AKUKUPEMPHERERANI

"Koma Iye chifukwa kuti akhala Iye nthawi yosatha ...komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira [kwathunthu] kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera [wakuwadyolera] iwo." —Ahebri 7:24, 25


INU NDI INE TIKHOZA KUKHALA NDI MOYO WOSATHA — 16

MOYO WOSATHA Kodi mukutsata njira yiti INUYO?

IMFA YOSATHA Yesu Kristu ndiye NJIRA ya ku MOYO wosatha pamodzi ndi Mulungu.

Mdierekezi (Satana) ndiye njira ya ku IMFA yosatha (chionongeko chamuyaya).

M'nyamata uyu akusankha bwino njira ya ku moyo wosatha.


KODI INU MUSANKHA NJIRA YITI? — 17

"Mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje...." —Yoswa 24:15b

"Potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu."—Deuteronomo 30:19b

YESU NDIYE NJIRA YA KU MOYO WOSATHA

"Ndipo palibe chipulumutso mwa wina aliyense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo."—Machitidwe 4:12

"Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha." —Yesaya 43:11


KODI NDI CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUSANKHA YESU NGATI TIFUNA MOYO WOSATHA? — 18-21

1. Kristu ndi amene adabwera.                                                                               "Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo...." —Yohane 10:10b

2. Kristu ndi amene anatikonda ndi kutifera ife.

"...Mwana wa Mulungu amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine." —Agalatiya 2:20b

Yesu adakhala munthu ndithu, wathupi ndi mwazi monga m'mene tilili ifemu.

"...kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo." —Ahebri 2:14b, 15

3. Ndi mwazi wa Yesu wokha umene ungatichotsere machimo athu.

"Pakuti wochita chotetezera [chotikhululukira] ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake." —Levitiko 17:11b

"Mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse." —1 Yohane 1:7b

"Amene tiri nao maomboledwe [chipulumutso] mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu." —Akolose 1:14

4. Kristu ndi amene anauka kwa akufa. 

"Podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu [ulamuliro] pa Iye." —Aroma 6:9 

"Ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka." —2 Akorinto 5:15 

Yesu anati, "Popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo." —Yohane 14:19b

5. Tiyenera kukhala ndi Mzimu wa Kristu mkati mwathu kuti tikaukitsidwe kunka ku moyo wosatha (kuti tikakhale mpaka muyaya).

"Kristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero." —Akolose 1:27c

"Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, [okhudzikawa] mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu." —Aroma 8:11

ONETSETSANI KUTI MZIMU WA KRISTU UKHALE MWA INU

"Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wake wa Kristu [sakhalanso mwa Kristu]". —Aroma 8:9b


M'MENE INU MUNGAPEZERE MOYO WOSATHA — 22

Tsatirani mfundo zofunika kutsatira kuyambira pa tsamba 24. 

"Ngakhale mwana adziwika ndi nchito zake." —Miyambo 20:11a 

Yesu amandikonda ine, ichi ndidziwa, popeza Buku Lopatulika limandiuza chomwecho.


YESU AMAKONDA ANA ONSE — 23

Koma Yesu anawaitana, nanena, "Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere." —Luka 18:16

"Chomwecho sichiri chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike [awonongedwe kapena akatayike mpaka muyaya]." —Mateyu 18:14

Zilibe kanthu kuti kaya ndinu ndani, kaya mumakhala kuti, chofunika kudziwa ndi chakuti Yesu amakukondani ndipo adakuferani inu. Yesu afunanso chikondi chanu. Mungathe kuonetsa chikondi chanu cha pa Yesu pomumvera Iye.

"Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga." —Yohane 14:15


M'MENE MUNGAPEZERE NJIRA YANU YA KWA MULUNGU — 24 - 28

1. Bvomerani kuti ndinu wochimwa (kuti simunamumvere Mulungu).

"Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu." —Aroma 3:23

2. Bwerani kwa Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu.

"Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu." —1 Timoteo 2:5

"Kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye." —Ahebri 7:25a

Yesu adati, "Wakudza kwa Ine sindidzamtaya [sindidzamponya] iye kunja." —Yohane 6:37b

3. Lapani machimo anu. 

(kulapa kutanthauza kumva chisoni kwambiri koleka nako kuchimwa.)

"Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu." —Machitidwe 3:19a

"Ambuye...aleza [augwira kapena aupoza] mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa." —2 Petro 3:9

4. Ululani machimo anu kwa Yesu.

(Kuulula ndiko kunena, kapena kubvomereza.) 

" Ngati tibvomereza machimo athu, ali wokhulu- pirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu." —1 Yohane 1:9a

Pa mizere ili pansiyi lembani ndime ya 1 Yohane 1:9 yomwe yalembedwa pa manja a munthu wopempherayo pa tsamba 25.

______________________________________________
______________________________________________
______________________________________________
______________________________________________

5. Tayani machimo anu.

(Kutaya ndiko kulekeratu, kusiyiratu.)

"Wobisa machimo ake sadzaona mwai; Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo." Miyambo 28:13

"Siyana nacho choipa, nuchite chokoma." Masalmo 37:27a

"Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro,...chiri mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense. Aefeso 2:8, 9 

6. Khulupirirani Yesu Kristu. 

"Ngati udzabvomereza m'kamwa mwako [kuti] Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka." Aroma 10:9

"Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako." Machitidwe 16:31

7. Landirani Yesu Kristu mu mtima ndi m'moyo mwanu.

Inu nokha ndi amene mungatsekule chitseko cha mtima wanu ndi kuitana Yesu kuti alowemo. Yesu anati, "Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine." Chibvumbulutso 3:20

"Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake. Yohane 1:12


M'MENE MUNGAPEMPHERERE — 29 

Ngati simunapempherepo ndipo mufuna thandizo kuti muzipemphera, mukhoza kutsata pemphero lili m'munsili monga ngati chitsanzo chanu: 

Okondedwa Ambuye Yesu, 

Ndikuthokozani pondifera pamtanda kundichotsera machimo anga. Ndili womva chisoni pa zolakwa zanga zonse zomwe ndachita. Ndikupemphani kuti chonde bwerani mumtima mwanga ndikukhalamo muyaya. Ndikukhulupirirani Inu tsopano lino kuti muyeretse mtima wanga. Ndikulandirani Inu kuti mukhale Ambuye ndi Mpulumutsi wangawanga. 

M'dzina la Yesu, Amen.


MUKAKHALA NDI YESU MUMTIMA MWANU,  MULI NAWO MOYO WOSATHA — 30

"Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene[wu] uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo." —1 Yohane 5:11b, 12a 

"Iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine,...wachokera kuimfa, nalowa m'moyo." —Yohane 5:24b 

Pamene thupi lanu lifa, ndi pamene mukhala ndi Ambuye (2 Akorinto 5:8). "Kristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero" (Akolose 1:27b). 

Ngati mwapempha Yesu kuti akukhululukireni machimo anu, ndipo mwakhulupirira Yesu Kristu monga Mpulumutsi wanu, lembani dzina lanu pamunsipa:


M'MENE MUNGASUNGIRE BWINO BWINO UDINDO WA KUTSATIRA YESU — 31

Werengani ndime za m'Buku Lopatulika (Mau a Mulungu) tsiku lililonse ndi kuwabisa mumtima mwanu pomaloweza ndime zina zomwe zimakuthandizani. (Zambiri mwa ndimezi zili m'kabuku kakang'ono kano.)

"Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso [chomwe inu mukhulupirira], chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo." —2 Timoteo 3:16


LANKHULANI KWA YESU MU PEMPHERO  NTHAWI YINA YILIYONSE — 32

Thokozani Yesu chifukwa cha zabwino zonse m'moyo mwanu. Muyamikeni chifukwa cha zinthu zonse zomwe wakuchitirani ndiponso chifukwa chopulumutsa moyo wanu. Pemphererani chosowa chanu china chilichonse. Pempherani m'dzina la Yesu.

"Ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera." —1 Yohane 5:14b

"Ndipo mupempherere wina kwa mnzake." —Yakobo 5:16b

"Ndi Kupempherera iwo akuzunza inu." —Mateyu 5:44b


PEMPHERO LIMENE YESU ADAPHUNZITSA OPHUNZIRA AKE — 33

(Wophunzira ndi munthu yemwe amatsata Yesu.)

Yesu anauza ophunzira ake kupemphera motere:

"Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire ife mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa, koma mutipulumutse ife kwa woipayo [chifukwa wanu uli ufumu ndi mphamvu ndi ulemerero, kwa nthawi zonse]." Amen. —Mateyu 6:9b-13

Pemphero ili liyenera kulowezedwa. Kawirikawiri, okhulupirira amapemphera pempheroli onse pamodzi mofuula.


MALAMULO KHUMI A MULUNGU AMATIPHUNZITSA — 34, 35
IFE MOMWE TINGAKHALIRE 
(Eksodo mutu 20) 

Anayi oyambawo ndi onena za chikondi chathu pa Mulungu 

1. "Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha." 

2. "Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chiri chonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba; ...usazipembedzere izo, usazitumikire izo." 

3. "Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe." 

4. "Uzikumbukila tsiku la Sabata, likhale lopatulika." 

Asanu ndi limodzi otsirizawo ndi onena za chikondi chathu pa munthu m'nzathu

MALAMULO KHUMI (KUPITIRIZIDWA) 

5. "Uzilemekeza atate ako ndi amako."

6. "Usaphe."

7. "Usachite chigololo." (Chigololo ndi kusakhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi m'banja.)

8. "Usabe."

9. "Usamnamizire mnzako."

10. "Usasirire...kanthu kali konse ka mnzako."

KUMVERA MULUNGU KUMABWERETSA MAYANKHO A MAPEMPHERO ATHU

"Ndipo chimene chiri chonse tipempha, tilandira kwa lye, chifukwa tisunga malamulo ake ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake." —1 Yoane 3:22


MALAMULO AWIRI AKULU ZEDI KUPOSA ONSE — 36

Chikondi chathu pa Mulungu 

1. Ndipo Yesu anati kwa iye, "Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse." Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba. —Mateyu 22:37, 38

Chikondi cha pa Munthu m'nzathu 

2. Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndiili, "Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini." —Mateyu 22:39 

Onse Malamulo Khumi (tsamba 34 ndi 35) ndi ophatikizidwa m'malamulo awiri akulu zedi aja.

CHIKONDI


CHIKONDI CHIPOSA ZINA ZONSE — 37, 38

Mutu Wodziwika Kwambiri Wa "Chikondi" 
(1 Akorinto 13:1-8, 13) 

"1Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. 2Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe chikondi, ndiri chabe. 3Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka [ndipatsa] thupi langa alitenthe m'moto, koma ndiribe chikondi, sindipindula kanthu ai. 4Chikondi chikhala chilezere [chimapilira], chiri chokoma mtima; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,5sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; 6sichikondwera ndi chinyengo [bodza], koma chikondwera ndi choonadi; 7chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. 8Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.... 13Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikuru cha izi ndicho chikondi.

MULUNGU NDI CHIKONDI

"Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye." —1 Yohane 4:16b


YESU AFUNA KUTI INU MUCHITIRE UMBONI KWA ENA — 39

(kunyumba, kusukulu, kutchalitchi, ndiponso pena paliponse)

Yesu anati, "Ndipo sanamlola, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikuru anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo." —Marko 5:19

 


MOMWE MUNGADZIWIRE MWANA  WAKE WENIWENI WA MULUNGU — 40, 41

"Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo." —Mateyu 7:20

"Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso." —Agalatiya 5:22, 23a

MWANA WENIWENI WA MULUNGU AMAKHULULUKIRA ENA 

"Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa [zochimwa] zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba." —Mateyu 6:14

ZINTHU ZISANU NDI ZIWIRI ZOMWE MULUNGU AMADANA NAZO 

"Maso akunyada, lilime lonama, Ndi manja akupha anthu osachimwa; Mtima woganizira ziwembu zoipa, Mapazi akuthamangira mphulupulu mmangu mmangu; Mboni yonama yonong'ona mabodza, Ndi wopikisanitsa abale." —Miyambo 6:17-19

Chipatso cha Mzimu

ZINTCHITO ZA THUPI: 

"...Ndizo dama, chodetsa [kukhala malo amodzi kwa anthu amene sali pa banja]...nyanga, madano, ndeu, ... zotetana, magawano,...kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; ...iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu." —Agalatiya 5:19-21 

...Kapena olobodoka ndi zoipa, ...kapena ambala, kapena osirira.   —1 Akorinto 6:9b, 10a

Zintchito za thupi

MULOLENI YESU AKUDZAZENI NDI MZIMU WAKE NAKUYERETSENI 

"Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, [mudapatulidwa]...m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu."  —1 Akorinto 6:11


NG'ANJO YAMOTO (HADE) NDI MALO ENIENI — 42

(Werengani Luka 16:19-26.)

Onetsetsani kuti mukukhulupirira mwa Yesu Kristu. Iye adzalemba dzina lanu m'Buku Lake Lamoyo.

"Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto." —Chibvumbulutso 20:15


YESU NDIYE NJIRA YOKHAYO YA KWA MULUNGU — 43

"Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene[wu] uli mwa Mwana wake."  —1 Yohane 5:11b

"Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu." —Aroma 6:23

"Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye." —Yohane 3:36

Yesu ananena naye, "Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine." —Yohane 14:6


KUMWAMBA NDI MALO ENIENI — 44

M'masomphenya a Yohane mu Chibvumbulutso 21 iye adaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, "Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano." —Chibvumbulutso 21:4, 5a

"...Mzindawo ngwa golidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera. Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu." —Chibvumbulutso 21:18b, 19b


YESU ANAPITA KUKAKONZA MALO OKHALAMO ONSE OKHULUPIRIRA MWA IYE — 45

"Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. M'nyumba ya Atate anga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso." —Yohane 14:1-3

FALITSANI UTHENGA WABWINOWU KWA ENA

Ndipo [Yesu] ananena nao, "Mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse." —Marko 16:15

Wokola mtima [wokopa ena] ali wanzeru. —Miyambo 11:30b


MALONJEZO A MULUNGU KWA ANA AKE — 46

"Pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu." —Ahebri 13:5b 

"Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, Akusunge m'nijira zako zonse." —Masalmo 91:11 

"Palibe wina angathe kuzikwatula m'dzanja la Atate." —Yohane 10:29b 

"Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimariziro cha nthawi ya pansi pano." —Mateyu 28:20b 

"Usaope zimene uti udzamve kuwawa; ...Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo." —Chibvumbulutso 2:10 

"Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe." —Yeremiya 33:3a


YESU AKUBWERANSO — 47 

Aliyense adzaukitsidwa kwa akufa. "Ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake, nadzaturukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza [kuchionongeko]." —Yohane 5:28b, 29 

Akufa mwa Kristu ndiwo amene adzauke poyamba. "Pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse." —1 Atesalonika 4:17 

 

"Dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake."   —Marko 13:33b


KODI YESU ADZABWERA MOTANI?  — 48

"Taonani adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya lye." —Chibvumbulutso 1:7a

Chenjerani ndi akristu onama ndi aneneri onama.

 "Munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze.  Onani, ali m'zipinda; musabvomereze." —Mateyu 24:23b, 26

YESU ALINKUBWERA POSACHEDWA
M'MITAMBO YA M'MWAMBA

"Mitundu yonse ya pa dziko lapansi iddzadziguguda pachifuwa...nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi ulemerero waukuru." —Mateyu 24: 30b


SALMO LA M'BUSA

(Masalmo 23)

"1Yehova ndiye m'busa wanga; sindidzasowa. 2Andigonetsa ku busa lamsipu: Anditsogolera ku madzi odikha. 3Atsitsimutsa moyo wanga; Anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. 

4Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, Sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine: Chibonga chanu ndi ndodo yanu izi zindisangalatsa ine. 5Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga: Mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka. 

6Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga: Ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse."


Kosindikizidwa ndi: 

Kaulele ­ Sikayenera kugulitsidwa kabukuka

If you are interested in receiving additional Scripture booklets, write to the publisher in English at the address below or order online:

World Missionary Press, Inc. 
P.O. Box 120 
New Paris, Indiana 46553-0120 U.S.A.


World Missionary Press Home Page | Go to the Top of This Page

Hit Counter